Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 25:23-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Dedani, ndi Tema, ndi Buzi, ndi onse amene ameta m'mbali mwa tsitsi;

24. ndi mafumu onse a Arabiya, ndi mafumu onse a anthu osanganizidwa okhala m'cipululu;

25. ndi mafumu onse a Zimiri, ndi mafumu onse a Elamu, ndi mafumu onse a Medi,

26. ndi mafumu onse a kumpoto, a kutari ndi a kufupi, wina ndi mnzace; ndi maufumu onse a dziko lapansi, okhala pansi pano; ndi mfumu ya Sesaki adzamwa pambuyo pao.

27. Ndipo uziti kwa iwo, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Imwani inu, ndi kuledzera, ndi kusanza, ndi kugwa, osanyamukanso konse, cifukwa ca lupanga limene ndidzatumiza mwa inu.

28. Ndipo padzakhala, ngati akana kutenga cikho pa dzanja lako kuti amwe, uziti kwa iwo, Yehova wa makamu atero: Kumwa muzimwa.

29. Pakuti, taonani, ndiyamba kucita coipa pa mudzi umene uchedwa ndi dzina langa, kodi inu mudzakhala osalangidwa konse? Simudzakhala osalangidwa; pakuti ndidzaitana lupanga ligwe pa onse okhala m'dziko lapansi, ati Yehova wa makamu.

30. Cifukwa cace muwanenere iwo mau onse awa, ndi kuti kwa iwo, Yehova adzabangula kumwamba, nadzachula mau ace mokhalamo mwace moyera; adzabangulitsira khola lace; adzapfuula, monga iwo akuponda mphesa, adzapfuulira onse okhala m'dziko lapansi.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 25