Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 25:10-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndiponso ndidzawacotsera mau akusekera ndi mau akukondwera, ndi mau a mkwati, ndi mau a mkwatibwi, mau a mphero, ndi kuwala kwa nyali.

11. Ndipo dziko lonseli lidzakhala labwinja, ndi cizizwitso, ndipo mitundu iyi idzatumikira mfumu ya ku Babulo zaka makumi asanu ndi awiri.

12. Ndipo kudzakhala, zitapita zaka makumi asanu ndi awiri, ndzidzalanga mfumu ya ku Babulo, ndi mtundu uja womwe, ati Yehova, cifukwa ca mphulupulu zao, ndi dziko la Akasidi; ndipo ndidzaliyesa mabwinja amuyaya.

13. Ndipo ndidzatengera dzikolo mau anga onse amene ndinanenera ilo, mau onse olembedwa m'buku ili, amene Yeremiya wanenera mitundu yonse.

14. Pakuti mitundu yambiri ndi mafumu akuru adzayesa iwo atumiki ao; ndipo ndidzabwezera iwo monga mwa macitidwe ao, monga mwa nchito ya manja ao.

15. Pakuti Yehova, Mulungu wa Israyeli, atero kwa ine, Tenga cikho ca vinyo wa ukaliwu pa dzanja langa, ndi kumwetsa mitundu yonse, imene ndikutumizirako.

16. Ndipo adzamwa, nadzayenda dzandi dzandi, nadzacita misala, cifukwa ca lupanga limene Ine ndidzatumiza mwa iwo.

17. Ndipo ndinatenga cikho pa dzanja la Yehova, ndinamwetsa mitundu yonse, imene Yehova ananditumizirako;

18. Yerusalemu, ndi midzi ya Yuda, ndi mafumu ace omwe, ndi akuru ace, kuwayesa iwo bwinja, cizizwitso, cotsonyetsa, ndi citemberero; monga lero lino;

19. Farao mfumu ya ku Aigupto, ndi atumiki ace, ndi akuru ace, ndi anthu ace onse;

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 25