Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 23:19-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Taonani, cimphepo ca Yehova, kupsa mtima kwace, kwaturuka, inde cimphepo cozungulira; cidzagwa pamutu pa woipa.

20. Mkwiyo wa Yehova sudzabwerera, mpaka atacita, mpaka atatha maganizo a mtima wace; masiku otsiriza mudzacidziwa bwino.

21. Sindinatuma aneneri awa, koma anathamanga; sindinanena ndi iwo, koma ananenera.

22. Koma akadaima m'upo wanga, akadamvetsa anthu anga mau anga, akadatembenuza iwo ku njira yao yoipa, ndi ku coipa ca nchito zao.

23. Kodi ndine Mulungu wa pafupi, ati Yehova, si Mulungu wa patari?

24. Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? ati Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? ati Yehova.

25. Ndamva conena aneneri, amene anenera zonama m'dzina langa, kuti, Ndalota, ndalota.

26. Ici cidzakhala masiku angati m'mtima mwa aneneri amene anenera zonama; ndiwo aneneri a cinyengo ca mtima wao?

27. amene aganizira kuti adzaiwalitsa anthu anga dzina langa, ndi maloto ao amene anena munthu yense kwa mnansi wace, monga makolo ao anaiwala dzina limene ndimcha nalo Baala.

28. Mneneri wokhala ndi loto, anene loto lace; ndi iye amene ali ndi mau anga, anene mau anga mokhulupirika. Kodi phesi ndi ciani polinganiza ndi tirigu? ati Yehova.

29. Kodi mau anga safanafana ndi moto? ati Yehova, ndi kufanafana ndi nyundo imene iphwanya mwala?

30. Cifukwa cace, taonani, Ine ndidana ndi aneneri, ati Yehova, amene amaba mau anga, yense kumbera mnansi wace.

31. Taonani, Ine ndidana ndi aneneri, ati Yehova, amene acita ndi malilime ao, ndi kuti, Ati Iye.

32. Taonani, Ine ndidana ndi amene anenera maloto onama, ndi kuwafotokoza ndi kusokeretsa anthu anga ndi zonama zao, ndi matukutuku ao acabe; koma Ine sindinatuma iwo, sindinauza iwo; sadzapindulira konse anthu awa, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 23