Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 21:6-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ndipo ndidzakantha okhalamo m'mudzi uwu, anthu ndi nyama, adzafa ndi caola cacikuru,

7. Ndipo pambuyo pace, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ace, ndi anthu, ngakhale a m'mudzi uwu amene asiyidwa ndi caola, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osacita cisoni, osacita cifundo.

8. Ndipo uziti kwa anthu awa, Yehova atero, Taonani, ndaika pamaso panu njira ya moyo ndi njira ya imfa.

9. Iye amene akhala m'mudzi uwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi caola; koma iye amene aturuka, napandukira kwa Akasidi akuzinga inu, adzakhala ndi moyo, ndipo moyo wace udzapatsidwa kwa iye ngati cofunkha.

10. Pakuti ndaika nkhope yanga pa mudzi uwu ndiucitire coipa, si cabwino, ati Yehova; ndipo udzapatsidwa m'dzanja la mfumu ya ku Babulo, ndipo iye adzautentha ndi moto.

11. Ndipo za nyumba ya mfumu ya Yuda, tamvani mau a Yehova:

12. Nyumba ya Davide iwe, Yehova atero, Cita ciweruzo m'mawa, ndi kumlanditsa amene afunkhidwa m'dzanja la wosautsa, kungaturuke kupsa mtima kwanga ngati moto, ndi kutentha kosazimika, cifukwa ca nchito zanu zoipa,

13. Taonani, Ine ndine mdani wako, iwe wokhala m'cigwa, ndi pa thanthwe la m'cidikha, ati Yehova; inu amene muti, Ndani adzatsikira kumenyana ndi ife? ndani adzalowa m'zokhalamo zathu?

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 21