Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 21:4-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Yehova, Mulungu wa Israyeli atero, Taonani, ndidzabweza zida za nkhondo zimene ziri m'manja anu, zimene mumenyana nazo ndi mfumu ya ku Babulo, ndi Akasidi akuzinga inu, kunja kwa malinga, ndipo ndidzazisonkhanitsa pakati pa mudzi uwu.

5. Ndipo Ine mwini ndidzamenyana ndi inu ndi dzanja lotambasuka ndi mkono wamphamvu, m'mkwiyo, ndi m'kupsya mtima, ndi m'ukali waukuru.

6. Ndipo ndidzakantha okhalamo m'mudzi uwu, anthu ndi nyama, adzafa ndi caola cacikuru,

7. Ndipo pambuyo pace, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ace, ndi anthu, ngakhale a m'mudzi uwu amene asiyidwa ndi caola, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osacita cisoni, osacita cifundo.

8. Ndipo uziti kwa anthu awa, Yehova atero, Taonani, ndaika pamaso panu njira ya moyo ndi njira ya imfa.

9. Iye amene akhala m'mudzi uwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi caola; koma iye amene aturuka, napandukira kwa Akasidi akuzinga inu, adzakhala ndi moyo, ndipo moyo wace udzapatsidwa kwa iye ngati cofunkha.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 21