Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 19:4-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Cifukwa andisiya Ine, nayesa malo ano acilendo, nafukizira m'menemo milungu yina, imene sanaidziwa, iwowa, ndi makolo ao ndi mafumu a Yuda: nadzaza malo ano ndi mwazi wa osacimwa;

5. namanga misanje ya Baala, kuti apsereze ana ao m'menemo nsembe zopsereza za Baala, cimene sindinawauza, sindinacinena, sicinalowa m'mtima mwanga;

6. cifukwa cace, taonani, masiku adza, ati Yehova kuti pamalo pano sipadzachedwanso Tofeti, kapena Cigwa ca mwana wace wa Hinomu, koma Cigwa Cophera anthu.

7. Ndipo ndidzataya uphungu wa Yuda ndi wa Yerusalemu m'malo ano; ndipo ndidzagwetsa iwo ndi lupanga pamaso pa adani ao, ndi pa dzanja la iwo amene afuna moyo wao; mitembo yao ndidzapatsa ikhale cakudya ca mbalame za m'mlengalenga, ndi ca zirombo za dziko lapansi.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 19