Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 17:3-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Iwe phiri langa la m'munda, ndidzapereka cuma cako ndi zosungidwa zako zikafunkhidwe, ndi misanje yako, cifukwa ca cimo, m'malire ako onse.

4. Iwe, iwe wekha, udzaleka pa colowa cako cimene ndinakupatsa iwe; ndipo ndidzakutumikiritsa adani ako m'dziko limene sulidziwa; pakuti wakoleza moto m'mkwiyo wanga umene udzatentha ku nthawi zamuyaya.

5. Atero Yehova: Wotembereredwa munthu amene akhulupirira munthu, natama mkono wanyama, nucoka kwa Yehova mtima wace.

6. Ndipo adzakhala ngati tsanya la m'cipululu, ndipo saona pamene cifika cabwino; koma adzakhala m'malo oumitsa m'cipululu, dziko lacikungu lopanda anthu.

7. Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene cikhulupiriro cace ndi Yehova.

8. Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuti madzi, wotambalitsa mizu yace pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lace likhala laliwisi; ndipo subvutika cakaca cirala, suleka kubala zipatso.

9. Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosaciritsika, ndani angathe kuudziwa?

10. Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa imso, kuti ndimpatse munthu yense monga mwa njira zace, monga zipatso za nchito zace.

11. Monga nkhwali iumatira pa mazira amene sinaikira, momwemo iye amene asonkhanitsa cuma, koma mosalungama; pakati pa masiku ace cidzamsiya iye, ndipo pa citsirizo adzakhala wopusa.

12. Malo opatulika athu ndiwo mpando wacifumu wa ulemerero, wokhazikika pamsanje ciyambire.

13. Inu Yehova, ciyembekezo ca Israyeli, onse amene akukusiyani Inu adzakhala ndi manyazi; onse ondicokera Ine adzalembedwa m'dothi, cifukwa asiya Yehova, kasupe wa madzi amoyo.

14. Mundiciritse ine, Yehova, ndipo ndidzaciritsidwa; mundipulumutse ine, ndipo ndidzapulumutsidwa; pakuti cilemekezo canga ndinu.

15. Taonani, ati kwa ine, Mau a Yehova ali kuti? adze tsopano.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 17