Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 16:13-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. cifukwa cace ndidzakuturutsani inu m'dziko muno munke ku dziko limene simunadziwa, kapena inu kapena makolo anu; pamenepo mudzatumikira milungu yina usana ndi usiku, kumene sindidzacitira inu cifundo.

14. Cifukwa cace, taonani, masiku adza, ati Yehova, kuti sadzanenanso, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israyeli kuwaturutsa m'dziko la Aigupto.

15. Koma, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israyeli kucokera ku dziko la kumpoto, ndi ku maiko ena kumene anawapitikitsirako; ndipo ndidzawabwezanso ku dziko lao limene ndinapatsa makolo ao.

16. Taonani, ndidzaitana akugwira nsomba ambiri, ati Yehova, ndipo adzawagwira iwo, pambuyo pace ndidzaitana osaka nyama ambiri, ndipo adzasaka iwo m'mapiri onse, ndi pa zitunda zonse, ndiponso m'mapanga a m'matanthwe.

17. Pakuti maso anga ali pa njira zao zonse, sabisika pa nkhope yanga, mphulupulu yao siibisika pamaso panga,

18. Poyamba ndibwezera mphulupulu yao ndi cimo lao cowirikiza; cifukwa anaipitsa dziko langa ndi mitembo ya zodetsedwa zao, nadzaza colowa canga ndi zonyansa zao.

19. Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kucokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira colowa ca bodza lokha, zopanda pace ndi zinthu zosapindula nazo.

20. Kodi munthu adzadzipangira yekha milungu, imene siiri milungu?

21. Cifukwa cace, taonani, ndidzadziwitsa iwo kamodzi aka, ndidzawadziwitsa dzanja langa ndi mphamvu yanga; ndipo adzadziwa kuti dzina langa ndine Yehova.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 16