Koma, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israyeli kucokera ku dziko la kumpoto, ndi ku maiko ena kumene anawapitikitsirako; ndipo ndidzawabwezanso ku dziko lao limene ndinapatsa makolo ao.