Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 14:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya onena za cirala.

2. Yuda alira, ndipo zipata zace zilefuka, zikhala pansi zobvekedwa ndi zakuda; mpfuu wa Yerusalemu wakwera.

3. Akuru ao atuma ang'ono ao kumadzi; afika kumaenje, osapeza madzi; abwera ndi mitsuko yao yopanda kanthu; ali ndi manyazi, athedwa nzeru, apfunda mitu yao.

4. Cifukwa ca nthaka yocita ming'aru, pakuti panalibe mvula padziko, olima ali ndi manyazi, apfunda mitu yao.

5. Inde, nswalanso ya m'thengo ibala nisiya ana ace, cifukwa mulibe maudzu.

6. Mbidzi zinaima pamapiri oti se, zipumira mphepo wefuwefu ngati ankhandwe; maso ao alema, cifukwa palibe maudzu.

7. Zingakhale zoipa zathu zititsutsa ife, citani Inu cifukwa ca dzina lanu, Yehova; pakuti zobwerera zathu zacuruka; takucimwirani Inu.

8. Inu, ciyembekezo ca Israyeli, mpulumutsi wace nthawi ya msauko, bwanji mukhala ngati mlendo m'dziko, ngati woyendayenda amene apatuka usiku?

9. Bwanji mukhala ngati munthu wodabwa, ngati munthu wamphamvu wosatha kupulumutsa? koma Inu, Yehova, muli pakati pathu, tichedwa ndi dzina lanu; musatisiye.

10. Atero Yehova kwa anthu awa, Comwecoakonda kusocerera; sanakaniza mapazi ao; cifukwa cace. Yehova sawalandira; tsopano adzakumbukira coipa cao, nadzalanga zocimwa zao.

11. Ndipo Yehova anati kwa ine, Usapempherere anthu awa zabwino.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 14