Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 13:16-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Lemekezani Yehova Mulungu wanu, kusanade, mapazi anu asanakhumudwe pa mapiri acizirezire; nimusanayembekeze kuunika, Ive asanasandutse kuunikaku mthunzi wa imfa, ndi kukuyesa mdima wa bii.

17. Koma ngati simudzamva, moyo wanga udzalira m'tseri cifukwa ca kunyada kwanu; diso langa lidzalira kwambiri, lidzagwa misozi, cifukwa zoweta za Yehova zagwidwa m'nsinga.

18. Nenani kwa mfumu ndi kwa amace wa mfumu, Dzicepetseni, khalani pansi; pakuti zapamtu zanu zagwa, korona wanu wokoma.

19. Midzi ya ku Mwera yatsekedwa, palibe wotsegulira. Yuda wonse wacotsedwa m'ndende wonsewo, wacotsedwa m'nsinga.

20. Tukulani maso anu, taonani iwo amene acokera kumpoto; ziri kuti zoweta zinapatsidwa kwa iwe, zoweta zako zokoma?

21. Udzanena ciani pamene adzaika abale ako akuru ako, pakuti iwe wekha wawalangiza iwo akukana iwe? kodi zowawa sizidzakugwira iwe monga mkazi wobala?

22. Ndipo ngati udzati m'mtima mwako, Zimenezi zandifikira ine cifukwa ninji? Cifukwa ca coipa cako cacikuru nsaru zako zoyesa mfula zasanduka mbudulira, ndi zithende zako zaphwetekwa.

23. Kodi angathe Mkusi kusanduliza khungu lace, kapena nyalugwe maanga ace? pamenepo mungathe inunso kucita zabwino, inu amene muzolowera kucita zoipa,

24. Cifukwa cace ndidzabalalitsa iwo, monga ziputu zakupita, ndi mphepo ya kucipululu.

25. Ici ndi cagwera cako, gawo la muyeso wako wa kwa Ine, ati Yehova; cifukwa wandiiwala Ine, ndi kukhulupirira zonama.

26. Cifukwa cace Ine ndidzaonetsa zotopola mikawo zako, pamaso pako, ndipo manyazi ako adzaoneka.

27. Ndaona zonyansa zako, ndi zigololo zako, ndi zakumemesa zako, ndi cinyerinyeri ca dama lako, pamapiri ndi m'munda. Tsoka kwa iwe, Yerusalemu! Sudzayeretsedwa; kodi zidzatero mpaka liti?

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 13