Ndipo ngati udzati m'mtima mwako, Zimenezi zandifikira ine cifukwa ninji? Cifukwa ca coipa cako cacikuru nsaru zako zoyesa mfula zasanduka mbudulira, ndi zithende zako zaphwetekwa.