Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 1:3-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Anamdzeranso masiku a Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kufikira Zedekiya mwana wace wa Yosiya mfumu ya Yuda atatsiriza zaka khumi ndi cimodzi; kufikira a ku Yerusalemu anatengedwa ndende mwezi wacisanu.

4. Ndipo anadza kwa ine mau a Yehova, kuti,

5. Ndisanakulenge iwe m'mimba ndinakudziwa, ndipo usanabadwe ndinakupatula iwe; ndinakuika kuti ukhale mneneri wa mitundu ya anthu.

6. Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Mulungu! taonani, sindithai kunena pakuti ndiri mwana.

7. Koma Yehova anati kwa ine, Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena conse cimene ndidzakuuza.

8. Usaope nkhope zao; cifukwa Ine ndiri ndi iwe kuti ndikulanditse iwe, ati Yehova.

9. Ndipo Yehova anaturutsa dzanja lace, na'khudza pakamwa panga; nati Yehova kwa ine, Taona ndaika mau anga m'kamwa mwako;

10. penyatu, lero ndakuika ulamulire mitundu ya anthu ndi maufumu, kuti uzule, upasule, uononge, ugwetse; umange, ubzyale.

11. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti, Yeremiya, uona ciani? Ndipo ndinati, Ine ndiona ntyole ya katungurume.

12. Ndipo Yehova anati kwa ine, Waona bwino pakuti Ine ndidzadikira mau anga kuwacita.

13. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yaciwiri, kuti, ona ciani? Ndipo ndinati, Ine ndiona mphika wogaduka; ndi pakamwa pace unafulatira kumpoto.

14. Ndipo Yehova anati kwa ine, Kucokera kumpoto coipa cidzaturukira onse okhala m'dziko.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 1