Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Rute 4:11-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Pamenepo anthu onse anali kucipata, ndi akuru, anati, Tiri mboni ife. Yehova acite kuti mkazi wakulowayo m'nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israyeli, iwo awiri; nucite iwe moyenera m'Efrata, numveke m'Betelehemu;

12. ndi nyumba yako inge nyumba ya Perezi, amene Tamare anambalira Yuda, ndi mbeu imene Yehova adzakupatsa ya namwali uyu.

13. Momwemo Boazi anatenga Rute, nakhala iye mkazi wace; ndipo analowa kwa iye; nalola Yehova kuti aime, ndipo anabala mwana wamwamuna.

14. Pamenepo akazi anati kwa Naomi, Adalitsike Yehova amene sana lola kuti akusowe woombolera lero; nilimveke dzina lace m'Israyeli,

15. Nakhale uyu wakukubwezera moyo, ndi wodyetsa ukalamba wako; pakuti mpongozi wako amene akukonda, amene aposa ana amuna asanu ndi awiri kukuthandiza, anambala.

16. Ndipo Naomi anamtenga mwanayo, namuika pacifuwa pace, nakhala mlezi wace.

17. Ndi akazi anansi ace anamucha dzina, ndi kuti, Kwa Naomi kwambadwira mwana; namucha dzina lace Ohedi; ndiye atate wa Jese atate wa Davide.

18. Iyo ndiyo mibadwo ya Perezi; Perezi anabala Hezironi;

19. ndi Hezironi anabala Ramu, ndi Ramu anabala Aminadabu;

20. ndi Aminadabu anabala Nasoni, ndi Nasoni anabala Salimoni;

21. ndi Salimoni anabala Boazi, ndi Boazi anabala Obedi;

22. ndi Obedi anabala Jese, ndi Jese anabala Davide.

Werengani mutu wathunthu Rute 4