Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Rute 1:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. NDIPO masiku akuweruza oweruzawo munali njala m'dziko. Ndipo munthu wa ku Betelehemu-Yuda anamuka nakagonera m'dziko la Moabu, iyeyu, ndi mkazi wace, ndi ana ace amuna awiri.

2. Dzina la munthuyo ndiye Elimeleki, ndi dzina la mkazi wace ndiye Naomi, ndi maina a ana ace awiri ndiwo Maloni, ndi Kilioni; ndiwo a ku Efrata ku Betelelehemu-Yuda. Iwowa ndipo analowa m'dziko la Moabu, nakhala komweko.

3. Ndipo Elimeleki mwamuna wace wa Naomi anamwalira; natsala iye ndi ana ace awiri.

4. Nadzitengera iwo akazi a ku Moabu; wina dzina lace ndiye Olipa, mnzace dzina lace ndiye Rute; ndipo anagonera komweko ngati zaka khumi.

5. Koma Maloni ndi Kilioni anamwalira onse awiri; motero ana ace amuna awiri ndi mwamuna wace anamsiya mkaziyo.

6. Pamenepo ananyamuka iyeyu ndi apongozi ace kuti abwerere kucoka m'dziko la Moabu; pakuti adamva m'dziko la Moabu kuti Yehova adasamalira anthu ace ndi kuwapatsa cakudya.

7. Naturuka iye kumene anakhalako ndi apongozi ace awiri pamodzi naye; namka ulendo wao kubwererakudzikola Yuda.

Werengani mutu wathunthu Rute 1