NDIPO masiku akuweruza oweruzawo munali njala m'dziko. Ndipo munthu wa ku Betelehemu-Yuda anamuka nakagonera m'dziko la Moabu, iyeyu, ndi mkazi wace, ndi ana ace amuna awiri.