Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Obadiya 1:11-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Tsiku lija unaima padera, tsiku lija alendo anagwira ndende makamu ace, nalowa m'zipata zace acilendo, nacitira Yerusalemu maere, iwenso unakhala ngati mmodzi wa iwowa.

12. Koma usapenyerera tsiku la mphwako, tsiku loyesedwa mlendo iye, nusasekerere ana a Yuda tsiku la kuonongeka kwao, kapena kuseka cikhakha tsiku lakupsinjika.

13. Usalowe m'mudzi wa anthu anga tsiku la tsoka lao, kapena kupenyerera iwe coipa cao tsiku la tsoka lao, kapena kuthira manja khamu lao tsiku la tsoka lao.

14. Ndipo usaime pamphambano kuononga opulumuka ace; kapena kupereka otsala ace tsiku lakupsinjika.

15. Pakuti tsiku la Yehova layandikira amitundu onse; monga unacita iwe, momwemo adzakucitira; cocita iwe cidzakubwererapamtupako.

16. Pakuti monga munamwa pa phiri langa lopatulika, momwemo amitundu onse adzamwa kosalekeza; inde adzamwa, nadzameza, nadzakhala monga ngati sanalipo.

17. Koma m'phiri la Ziyoni mudzakhala opulumuka, ndipo lidzakhala lopatulika; ndi a nyumba ya Yakobo adzakhala nazo zolowa zao.

18. Ndipo nyumba ya Yakobo idzakhala moto, ndi nyumba ya Yosefe lawi, ndi nyumba ya Esau ngati ciputu, ndipo adzawatentha pakati pao, ndi kuwapsereza; ndipo sadzakhalapo otsalira nyumba ya Esau; pakuti Yehova wanena.

19. Ndipo akumwela adzakhala nalo phiri la Esau colowa cao; ndi iwo a kucidikha adzakhala nalo dziko la Afilisti; ndipo adzakhala nayo minda ya Efraimu, ndi minda ya Samariya colowa cao; ndi Benjamini adzakhala nalo la Gileadi.

20. Ndipo andende a khamu ili la ana a Israyeli, okhala mwa Akanani, adzakhala naco colowa cao mpaka pa Zarefati; ndi andende a ku Yerusalemu okhala m'Sefaradi adzakhala nayo midzi ya kumwela, colowa cao.

21. Ndipo apulumutsi adzakwera pa phiri la Ziyoni kuweruza phiri la Esau; ndipo ufumu udzakhala wace wa Yehova.

Werengani mutu wathunthu Obadiya 1