Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nyimbo 4:2-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Mano ako akunga gulu la nkhosa zosengasenga,Zokwera kucokera kosamba;Yonse iri ndi ana awiri,Palibe imodzi yopoloza.

3. Milomo yako ikunga mbota yofiira,M'kamwa mwako ndi kukoma:Palitsipa pako pakunga phande la khangazaPatseri pa cophimba cako.

4. Khosi lako likunga nsanja ya Davide anaimangira zida,Apacikapo zikopa zikwi,Ngakhale zikopa zonse za amuna amphamvu,

5. Maere ako awiri akunga ana awiri a nswala obadwa limodzi,Akudya pakati pa akakombo.

6. Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha,Ndikamuka ku phiri la nipa,Ndi ku citunda ca mtanthanyerere.

7. Wakongola monse monse, wokondedwa wanga, namwaliwe,Mulibe cirema mwa iwe.

8. Idza nane kucokera ku Lebano, mkwatibwi,Kucokera nane ku Lebano:Unguza pamwamba pa Amana,Pa nsonga ya Seniri ndi Hermoni,Pa ngaka za mikango,Pa mapiri a anyalugwe.

9. Walanda mtima wanga, mlongwanga, mkwatibwi;Walanda mtima wanga ndi diso lako limodzi,Ndi cinganga cimodzi ca pakhosi pako,

10. Ha, cikondi cako ncokongola, mlongwanga, mkwatibwi!Kodi cikondi cako siciposa vinyo?Kununkhira kwa mphoka yako ndi kuposa zonunkhiritsa za mitundu mitundu!

Werengani mutu wathunthu Nyimbo 4