Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 9:4-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndipo Mose ananena ndi ana a Israyeli, kuti acite Paskha.

5. Ndipo anacita Paskha mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi cinai la mweziwo, madzulo, m'cipululu ca Sinai; monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo ana a Israyeli anacita.

6. Pamenepo panali amuna, anadetsedwa ndi mtembo wa munthu, ndipo sanakhoza kucita Paskha tsiku lomwelo; m'mwemo anafika pamaso pa Mose ndi pamaso pa Aroni tsiku lomwelo;

7. nanena naye amunawa, Tadetsedwa ife ndi mtembo wa munthu; atiletseranji, kuti tisabwere naco copereka ca Yehova pa nyengo yace yoikidwa, pakati pa ana a Israyeli?

8. Ndipo Mose ananena nao, Baimani; ndimve couza Yehova za inu.

9. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

10. Nena ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Angakhale munthu wa inu kapena wa mibadwo yanu, adetsedwa, cifukwa ca mtembo, kapena pokhala paulendo, koma azicitira Yehova Paskha.

11. Mwezi waciwiri, tsiku lace lakhumi ndi cinai, madzulo, aucite; audye ndi mkate wopanda cotupitsa ndi msuzi wowawa.

12. Asasiyeko kufikira m'mawa, kapena kuthyolapo pfupa; aucite monga mwa lemba lonse la Paskha.

13. Munthu akakhala woyera, wosakhala paulendo, koma akaleka kucita Paskha, amsadze munthuyo kwa anthu a mtundu wace; popeza sanabwera naco copereka ca Yehova pa nyengo yace yoikidwa, munthuyu asenze kucimwa kwace.

14. Ndipo mlendo akakhala mwa inu, nakacitira Yehova Paskha, azicita monga mwa lemba la Paskha, ndi monga mwa ciweruzo cace; lemba likhale limodzi kwa inu, ndi kwa mlendo, ndi kwa wobadwa m'dziko.

15. Ndipo tsiku loutsa kacisi mtambo unaphimba kacisi, ndiwo cihema cokomanako; ndipo madzulo padaoneka pakacisi ngati moto, kufikira m'mawa.

Werengani mutu wathunthu Numeri 9