Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 9:15-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo tsiku loutsa kacisi mtambo unaphimba kacisi, ndiwo cihema cokomanako; ndipo madzulo padaoneka pakacisi ngati moto, kufikira m'mawa.

16. Kudatero kosalekeza; mtambo umaciphimba, ndimoto umaoneka usiku,

17. Ndipo pokwera mtambo kucokera kucihema, utatero ana a Israyeli amayenda ulendo wao; ndipo pamalo pokhala mtambo, pamenepo ana a Israyeli amamanga mahema ao.

18. Pakuwauza Yehova ana a Israyeli amayenda ulendo, powauza Yehova amamanga mahema ao; masiku onse mtambo ukakhala pamwamba pa kacisi amakhala m'cigono.

19. Ndipo pakukhalitsa mtambo masiku ambiri pamwamba pa kacisi, pamenepo ana a Israyeli anasunga udikiro wa Yehova osayenda ulendo.

20. Ndipo pokhala mtambo pamwamba pa kacisi masiku pang'ono; pamenepo anakhala m'cigono monga awauza Yehova, nayendanso ulendo monga anauza Yehova.

21. Koma mtambo ukakhala kuyambira madzulo kufikira m'mawa; pokwera mtambo m'mawa, ayenda ulendo; ngakhale msana ngakhale usiku, pokwera mtambo, ayenda ulendo.

22. Ngakhale masiku awiri, kapena mwezi, kapena masiku ambiri, pokhalitsa mtambo pamwamba pa kacisi ndi kukhalapo, ana a Israyeli anakhala m'cigono, osayenda ulendo; koma pakukwera uwu, anayenda ulendo.

23. Powauza Yehova amanga mahema, powauza Yehova ayenda ulendo; anasunga udikiro wa Yehova powauza Yehova mwa dzanja la Mose.

Werengani mutu wathunthu Numeri 9