Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 8:19-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo ndapereka Alevi akhale mphatso ya kwa Aroni ndi ana ace amuna yocokera mwa ana a Israyeli, kucita nchito ya ana a Israyeli, m'cihema cokomanako ndi kucita cotetezera ana a Israyeli; kuti pasakhale mliri pakati pa ana a Israyeli, pakuyandikiza ana a Israyeli ku malo opatulika.

20. Ndipo Mose ndi Aroni ndi khamu lonse la ana a Israyeli anacitira Alevi monga mwa zonse Yehova adauza Mose kunena za Alevi; momwemo ana a lsrayeli anawacitira.

21. Ndipo Alevi anadziyeretsa, natsuka zobvala zao; ndi Aroni anawapereka ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndi Aroni anawacitira cotetezera kuwayeretsa.

22. Ndipo atatero, Alevi analowa kucita Debito yao m'cihema cokomanako pamaso pa Aroni, ndi pamaso pa ana ace amuna; monga Yehova anauza Mose kunena za Alevi, momwemo anawacitira.

23. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

24. Ici ndi ca Alevi: kuyambira ali wa zaka makumi awiri ndi zisanu ndi mphambu azilowa kutumikira utumikiwu mu nchito ya cihema cokomanako;

25. ndipo kuyambira zaka makumi asanu azileka kutumikira utumikiwu, osacitanso nchitoyi;

26. koma atumikire pamodzi ndi abale ao m'cihema cokomanako, kusunga udikirowo, koma osagwira nchito. Utere nao Alevi kunena za udikiro wao.

Werengani mutu wathunthu Numeri 8