15. Ndipo atatero alowe Alevi kucita Debito ya cihema cokomanako; ndipo uwayeretse, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula.
16. Pakuti aperekedwa konse kwa Ine ocokera mwa ana a Israyeli; ndadzitengera iwo m'malo mwa onse akutsegula m'mimba, ndiwo oyamba kubadwa a ana a Israyeli.
17. Pakuti a oyamba kubadwa onse mwa ana a Israyeli ndi anga, mwa anthu ndi zoweta; tsiku lija ndinakantha oyamba kubadwa onse m'dziko la Aigupto, ndinadzipatulira iwo akhale anga.
18. Ndipo ndatenga Alevi m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israyeli.
19. Ndipo ndapereka Alevi akhale mphatso ya kwa Aroni ndi ana ace amuna yocokera mwa ana a Israyeli, kucita nchito ya ana a Israyeli, m'cihema cokomanako ndi kucita cotetezera ana a Israyeli; kuti pasakhale mliri pakati pa ana a Israyeli, pakuyandikiza ana a Israyeli ku malo opatulika.
20. Ndipo Mose ndi Aroni ndi khamu lonse la ana a Israyeli anacitira Alevi monga mwa zonse Yehova adauza Mose kunena za Alevi; momwemo ana a lsrayeli anawacitira.
21. Ndipo Alevi anadziyeretsa, natsuka zobvala zao; ndi Aroni anawapereka ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndi Aroni anawacitira cotetezera kuwayeretsa.
22. Ndipo atatero, Alevi analowa kucita Debito yao m'cihema cokomanako pamaso pa Aroni, ndi pamaso pa ana ace amuna; monga Yehova anauza Mose kunena za Alevi, momwemo anawacitira.
23. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
24. Ici ndi ca Alevi: kuyambira ali wa zaka makumi awiri ndi zisanu ndi mphambu azilowa kutumikira utumikiwu mu nchito ya cihema cokomanako;
25. ndipo kuyambira zaka makumi asanu azileka kutumikira utumikiwu, osacitanso nchitoyi;