Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 30:7-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. nakazimva mwamuna wace, nakakhala naye cete tsiku lakuzimva iye; pamenepo zowinda zace zidzakhazikika, ndi zodziletsa anamanga nazo moyo wace zidzakhazikika.

8. Kama mwamuna wace akamletsa tsiku lakumva iye; pamenepo adzafafaniza cowinda cace anali naco, ndi zonena zopanda pace za milomo yace, zimene anamanga nazo moyo wace; ndipo Yehova adzamkhululukira.

9. Koma cowinda ca mkazi wamasiye, kapena mkazi wocotsedwa, ziti zonse anamanga nazo moyo wace zidzamkhazikikira.

10. Ndipo ngati anawinda m'nyumba ya mwamuna wace, kapena anamanga moyo wace ndi codziletsa ndi kulumbirapo,

11. ndipo mwanuna wace anamva, koma anakhala naye cete osamletsa, pamenepo zowinda zace zonse zidzakhazikika, ndi zodziletsa zonse anamanga nazo moyo wace zidzakhazikika.

12. Koma ngati mwamuna wace anazifafanizadi tsiku lakuzimva iye, zonse zoturuka m'milomo yace kunena za zowinda zace, kapena za codziletsa ca moyo wace sizidzakhazikika; mwamuna wace anazifafaniza; ndipo Yehova adzamkhululukira Iye.

13. Cowinda ciri conse, ndi columbira ciri conse codziletsa cakucepetsa naco moyo, mwamuna wace acikhazikira, kapena mwamuna wace acifafaniza.

14. Koma mwamuna wace akakhala naye cete tsiku ndi tsiku; pamenepo akhazikira zowinda zace zonse, kapena zodziletsa zace zonse, ziri pa iye; wazikhazikitsa, popeza anakhala naye cete tsikuli anazimva iye.

15. Koma akazifafaniza atatha kuzimva; pamenepo adzasenza mphulupulu yace.

16. Awa ndi malemba amene Yehova analamulira Mose, a pakati pa mwamuna ndi mkazi wace, pakati pa atate ndi mwana wace wamkazi, akali namwali, m'nyumba ya atate wace.

Werengani mutu wathunthu Numeri 30