Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 3:33-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Banja la Amali, ndi banja la Amusi ndiwo a Merari; ndiwo mabanja a Merari.

34. Ndipo owerengedwa ao, powerenga amuna onse, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu, ndiwo zikwi zisanu ndi cimodzi kudza mazana awiri.

35. Ndi kalonga wa nyumba ya makolo ya mabanja a Merari ndiye Zuriyeli mwana wa Abiyaili; azimanga mahema ao pa mbali ya kacisi ya kumpoto.

36. Ndipo coyang'anira iwo, udikiro wao wa ana a Merari ndiwo matabwa a kacisi, ndi mitanda yace, ndi mizati ndi nsanamira zace, ndi makamwa ace, ndi zipangizo zace zonse, ndi nchito zace zonse;

37. ndi nsici za pabwalo pozungulira, ndi makamwa ace, ndi ziciri zace, ndi zingwe zace.

38. Ndipo amene adamanga mahema ao pa khomo la kacisi, kum'mawa, pa khomo la cihema cokomanako koturukira dzuwa, ndiwo Mose ndi Aroni, ndi ana ace amuna, akusunga udikiro wa malo opatulika, ndiwo udikiro wa ana a Israyeli; koma mlendo wakuyandikizako amuphe,

39. Owerengedwa onse a Alevi, adawawerenga Mose ndi Aroni, powauza Yehova, monga mwa mabanja ao, amuna onse kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu, ndiwo zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.

40. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Werenga amuna oyamba kubadwa onse a ana a Israyeli kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu nuone ciwerengo ca maina ao.

41. Ndipo unditengere Ine Alevi (ine ndine Yehova) m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israyeli; ndi ng'ombe za Alevi m'malo mwa zoyamba kubadwa zonse mwa ng'ombe za ana a Israyeli.

42. Ndipo Mose anawawerenga, monga Yehova adamuuza, oyamba kubadwa onse mwa ana a Israyeli.

43. Ndipo amuna onse oyamba kubadwa, powerenga maina, kuyambira a mwezi umodzi ndi mphambu, owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana awiri ndi makumi asanu ndi awiri mphambu atatu.

44. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

Werengani mutu wathunthu Numeri 3