Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 26:48-65 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

48. Ana amuna a Nafitali monga mwa mabanja ao ndiwo: Yazeli, ndiye kholo la banja la Ayazeli; Guni, ndiye kholo la banja la Aguni;

49. Yezeri, ndiye kholo la banja la Ayezeri; Silemu, ndiye kholo la banja la Asilemu.

50. Iwo ndiwo mabanja a Nafitali, monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana anai.

51. Iwo ndiwo owerengedwa ao a ana a Israyeli, zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu cimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu.

52. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

53. Dziko ligawikire iwowa monga mwa kuwerenga kwa maina, likhale colowa cao.

54. Ocurukawo, uwacurukitsire colowa cao; ocepawo uwacepetsere colowa cao; ampatse yense colowa cace monga mwa owerengedwa ace.

55. Koma aligawe ndi kucita maere; colowa cao cikhale monga mwa maina a mafuko a makolo ao,

56. Agawire ocuruka ndi ocepa colowa cao monga mwa kucita maere.

57. Ndipo awa ndi owerengedwa ao a Alevi monga mwa mabanja ao: Gerisoni, ndiye kholo la banja la Agerisoni; Kohati, ndiye kholo la banja la Akohati; Merari, ndiye kholo la banja la Amerari.

58. Awa ndi mabanja a Alevi: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amali, banja la Amusi, banja la Akohati. Ndipo Kohati anabala Amiramu.

59. Ndipo dzina lace la mkazi wace wa Amiramu ndiye Yokebedi, mwana wamkazi wa Levi, wobadwira Levi m'Aigupto; ndipo iye anambalira Amiramu Aroni ndi Mose, ndi Miriamu mlongo wao.

60. Ndipo Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi ltamara anabadwira Aroni.

61. Koma Nadabu ndi Abihu adafa, muja anabwera nao moto wacilendo pamaso pa Yehova.

62. Ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi awiri mphambu zitatu, mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu; popeza sanawerengedwa pakati pa ana a Israyeli; cifukwa sanawapatsa colowa mwa ana a Israyeli.

63. Iwo ndiwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eleazara wansembe, amene anawerenga ana a Israyeli m'zidikha za Moabu ku Yordano pafupi pa Yeriko.

64. Koma pakati pao panalibe mmodzi wa iwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Aroni wansembe, amene anawerenga ana a Israyeli m'cipululu ca Sinai.

65. Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'cipululu. Ndipo sanatsalira mmodzi wa iwowa koma Kalebi mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.

Werengani mutu wathunthu Numeri 26