Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 21:23-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ndipo Sihoni sanalola Israyeli apitire m'malire ace; koma Sihoni anamemeza anthu ace onse, nadzakomana naye Israyeli m'cipululu, nafika ku Jahazi, nathira nkhondo pa Israyeli.

24. Ndipo Israyeli anamkantha ndi lupanga lakuthwa, nalanda dziko lace likhale lao lao, kuyambira Arinoni kufikira Yaboki, kufikira ana ai Amoni; popeza malire a ana a Amoni ndiwo olimba.

25. Ndipo Israyeli analanda midzi iyi yonse; nakhala Israyeli m'midzi yonse ya Aamori; m'Hesiboni ndi miraga yace yonse.

26. Popeza Hesiboni ndiwo mudzi wa Sihoni mfumu ya Aamori, imene idathira nkhondo pa mfumu idafayo ya Moabu, nilanda dziko lace m'dzanja lace kufikira Arinoni.

27. Cifukwa cace iwo akunena mophiphiritsa akuti,Idzani ku Hesiboni,Mudzi wa Sihoni umangike, nukhazikike:

28. Popeza moto unaturuka m'Hesiboni,Cirangali ca mota m'mudzi wa Sihoni;Catha Ari wa Moabu,Eni misanje ya Arinoni.

29. Tsoka kwa iwe, Moabu!Mwaonongeka, anthu a Kemosi inu,Anapereka ana ace amuna opulumuka,Ndi ana ace akazi akhale ansinga,Kwa Sihoni mfumu ya Aamori.

30. Tinawagwetsa; Hesiboni waonongeka kufikira ku Diboni,Ndipo tinawapululutsa kufikira ku Nofa,Ndiwo wakufikira ku Medeba.

31. Comweco Israyeli anakhala m'dziko la Aamori.

32. Ndipo Mose anatumiza anthu akazonde Yazere, nalanda miraga yace, napitikitsa Aamori a komweko.

33. Ndipo anatembenuka nakwera kudzera njira ya ku Basanu; ndipo Ogi mfumu ya ku Basana anaturuka kukumana nao, iye ndi anthu ace onse, kudzacita nao nkhondo ku Edreyi.

34. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Usamuopa; popeza ndampereka m'manja mwako, iye ndi anthu ace onse, ndi dziko lace; umcitire monga umo unacitira Sihoni mfumu ya Aamori anakhalayo ku Hesiboni.

35. Ndipo anamkantha iye, ndi ana ace amuna ndi anthu ace onse, kufikira sanatsala ndi mmodzi yense; nalanda dziko lace likhale lao lao.

Werengani mutu wathunthu Numeri 21