Ndipo anatembenuka nakwera kudzera njira ya ku Basanu; ndipo Ogi mfumu ya ku Basana anaturuka kukumana nao, iye ndi anthu ace onse, kudzacita nao nkhondo ku Edreyi.