Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 20:19-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo ana a Israyeli ananena naye, Tidzatsata mseu; ndipo tikakamwa madzi ako, ine ndi zoweta zanga, pamenepo ndidzapatsa mtengo wace; sindifuna kanthu kena koma kungopitapo mwa njira.

20. Koma anati, Usapitirepo. Ndipo Edomu anaturukira kukumana naye ndi anthu ambiri, ndi dzanja lamphamvu.

21. Potero Edomu anakana kulola Israyeli kupitira pa malire ace; cifukwa cace Aisrayeli anampatukira.

22. Ndipo anayenda ulendo kucokera ku Kadesi; ndi ana a Israyeli, ndilo khamu lonse, anadza ku phiri la Hori.

23. Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni m'phiri la Hori, pa malire a dziko la Edomu, ndi kuti,

24. Aroni adzaitanidwa kumka kwa anthu a mtundu wace; pakuti sadzalowa m'dziko limene ndapatsa ana a Israyeli, popeza munapikisana ndi mau anga ku madzi a Meriba.

25. Tenga Aroni ndi Eleazara mwana wace, nukwere nao m'phiri la Hori;

26. nubvule Aroni zobvala zace, numbveke Eleazara mwana wace; ndipo Aroni adzaitanidwa kumka kwa anthu a mtundu wace, nadzafa komweko.

27. Pamenepo Mose anacita monga adamuuza; ndipo anakwera m'phiri la Hori pamaso pa khamu lonse.

28. Ndipo Mose anabvula Aroni zobvala zace, nabveka Eleazara mwana wace; ndipo Aroni anafa pomwepo pamwamba pa phiri, Pamenepo Mose ndi Eleazara anatsika m'phirimo.

29. Pamene khamu lonse linaona kuti Aroni adamwalira, anamlira Aroni masiku makumi atatu, ndiyo mbumba yonse ya Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Numeri 20