Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 19:13-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ali yense wakukhudza mtembo wa munthu ali yense wakufa, osadziyeretsa, aipsa kacisi wa Yehova; amsadze munthuyo kwa Israyeli; popeza sanamwaza madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa; kudetsedwa kwace kukali pa iye.

14. Cilamulo ndi ici: Munthu akafa m'hema, yense wakulowa m'hemamo, ndi yense wakukhala m'hemamo, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.

15. Ndi zotengera zonse zobvundukuka, zopanda cibvundikilo comangikapo, ziri zodetsedwa.

16. Ndipo ali yense wakukhudza munthu wophedwa ndi lupanga, kapena mtembo, kapena pfupa la munthu, kapena manda, pathengo poyera, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.

17. Ndipo atengereko wodetsedwayo mapulusa akupsererawo a nsembe yaucimo, nathirepo m'cotengera madzi oyenda;

18. ndi munthu woyera atenge hisope, nambviike m'madzimo, ndi kuwawaza pahema ndi pa zotengera zonse, ndi pa anthu anali pomwepo, ndi pa iye wakukhudza pfupa, kapena wophedwa, kapena wakufa, kapena Manda.

19. Ndipo woyerayo awaze pa wodetsedwayo tsiku lacitatu, ndi tsiku lacisanu ndi ciwiri; ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri amyeretse; ndipo atsuke zobvala zace, nasambe m'madzi, nadzakhala woyera madzulo.

20. Koma munthu wakukhala wodetsedwa, koma wosadziyeretsa, azimsadza munthuyo pakati pa msonkhano, popeza waipsa malo opatulika a Yehova; sanamwaza madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa.

21. Ndipo likhale kwa iwo lemba losatha; kuti iye wakuwaza madzi akusiyanitsa azitsuka zobvala zace; ndi iye wakukhudza madzi akusiyanitsa adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

22. Ndipo ciri conse munthu wodetsedwa acikhudza cidzakhala codetsedwa; ndi munthu wakucikhudza adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.

Werengani mutu wathunthu Numeri 19