Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 19:10-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo wakuola mapulusayo a ng'ombe ya msoti atsuke zobvala zace, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; ndipo likhale lemba losatha kwa ana a Israyeli, ndi kwa mlendo wakukhala pakati pao.

11. Iye wakukhudza mtembo wa munthu ali yense adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri;

12. iyeyo adziyeretse nao tsiku lacitatu, ndi pa tsiku lacisanu ndi ciwiri adzakhala woyera; koma akapanda kudziyeretsa tsiku lacitatu, sadzakhala woyera tsiku lacisanu ndi ciwiri.

13. Ali yense wakukhudza mtembo wa munthu ali yense wakufa, osadziyeretsa, aipsa kacisi wa Yehova; amsadze munthuyo kwa Israyeli; popeza sanamwaza madzi akusiyanitsa; ndiye wodetsedwa; kudetsedwa kwace kukali pa iye.

14. Cilamulo ndi ici: Munthu akafa m'hema, yense wakulowa m'hemamo, ndi yense wakukhala m'hemamo, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.

15. Ndi zotengera zonse zobvundukuka, zopanda cibvundikilo comangikapo, ziri zodetsedwa.

16. Ndipo ali yense wakukhudza munthu wophedwa ndi lupanga, kapena mtembo, kapena pfupa la munthu, kapena manda, pathengo poyera, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri.

Werengani mutu wathunthu Numeri 19