Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 18:3-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo asunge udikiro wako, ndi udikiro wa cihema conse; koma asayandikize zipangizo za malo opatulika, ndi guwa la nsembe, kuti mungafe, iwo ndi inu.

4. Koma aziphatikana nawe, nazisunga udikiro wa cihema cokomanako, kucita nchito yonse ya cihema; koma mlendo asayandikize inu.

5. Ndipo musunge udikiro wa malo opatulika, ndi udikiro wa guwa la nsembe; kuti pasakhalenso mkwiyo pa ana a Israyeli.

6. Ndipo Ine, taonani, ndinatenga abale anu Alevi kuwacotsa pakati pa ana a Israyeli; ndiwo mphatso yanu, yopatsidwa kwa Yehova, kucita nchito ya cihema cokomanako.

7. Ndipo iwe ndi ana ako amuna pamodzi ndi iwe mucite nchito yanu ya nsembe, pa zonse za ku guwa la nsembe, ndi za m'kati mwa nsaru yocinga; ndipo mutumikire; ndikupatsani nchito yanu ya nsembe, utumiki wopatsika kwaulere; koma mlendo wakuyandikiza amuphe.

8. Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ndipo taona, Ine ndakupatsa udikiro wa nsembe zanga zokweza, ndizo zopatulika zonse za ana a Israyeli; cifukwa ca kudzozedwaku ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna, likhale lemba losatha.

Werengani mutu wathunthu Numeri 18