Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 18:25-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Ndipo Yehova ananena ndil Mose, nati,

26. Unenenso ndi Alevi, nuti nao, Pamene mulandira kwa ana a Israyeli, limodzi la magawo khumi limene ndakupatsani likhale colowa canu cocokera kwao, muziperekako nsembe yokweza ya Yehova, limodzi la magawo khumi la limodzi la magawo khumi.

27. Ndipo akuyesereninso nsembe yanu yokweza monga tirigu wa padwale, monga mopondera mphesa modzala.

28. Momweno inunso muzipereka kwa Yehova nsembe yokweza yocokera ku magawo anu onse a magawo khumi, a zonse muzilandira kwa ana a Israyeli; ndipo muperekeko nsembe yokweza ya Yehova kwa Aroni wansembe.

29. Mupereke nsembe zokweza zonse za Yehova kuzitenga ku mphatso zanu zonse, kusankhako zokometsetsa ndizo zopatulika zace.

30. Cifukwa cace unene nao, Pamene mukwezako zokometsetsa zace, zidzayesedwanso kwa Alevi ngati zipatso za padwale, ndi zipatso za mopondera mphesa,

31. Ndipo muzidye pamalo ponse, inu ndi a pabanja panu; popeza ndizo mphotho yanu mwa nchito yanu m'cihema cokomanako.

32. Ndipo simudzasenzapo ucimo, mutakwezako zokometsetsa zace; ndipo musamaipsa zinthu zopatulika za ana a Israyeli, kuti mungafe.

Werengani mutu wathunthu Numeri 18