Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 18:15-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ziri zonse zoyambira kubadwa mwa zamoyo zonse zimene abwera nazo kwa Yehova, mwa anthu ndi mwa nyama, ndi zako; koma munthu woyamba kubadwa uzimuombola ndithu; ndi nyama yodetsa yoyamba kubadwa uziiombola.

16. Ndipo zimene ziti zidzaomboledwa uziombole kuyambira za rowezi umodzi, monga mwa kuyesa kwako, pa ndarama za masekeli asanu, kuyesa sekeli wa malo opatulika, ndiwo magera makumi awiri.

17. Koma ng'ombe yoyamba kubadwa, kapena nkhosa yoyamba kubadwa, kapena mbuzi yoyamba kubadwa, usaziombola; ndizo zopatulika; uwace mwazi wace pa guwa la nserobe, ndi kufukiza mafuta ao, nsembe yamoto ya pfungo lokoma kwa Yehova.

18. Ndipo nyama yace ndi yako, ndiyo nganga ya nsembe yoweyula ndi mwendo wathako wa kulamanja, ndizo zako.

19. Nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika, zimene ana a Israyeli azikweza kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako amuna ndi kwa ana ako akazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; ndilo pangano lamcere losatha, pamaso pa Yehova, kwa iwe ndi mbeu zako pamodzi ndi iwe.

20. Ndipo Yehova ananena ndi Aroni, Ulibe colowa m'dziko lao, ulibe gawo pakati pao; Ine ndine gawo lako ndi colowa cako pakati pa ana a Israyeli.

21. Ndipo taonani, ndawaninkha ana a Levi limodzi la magawo khumi mwa zonse m'Israyeli, likhale colowa cao, mphotho ya pa nchito yao alikuicita, nchito ya cihema cokomanako.

22. Ndipo kuyambira tsopano ana a Israyeli asayandikize cihema cokomanako, angamasenze ucimo kuti angafe.

Werengani mutu wathunthu Numeri 18