Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 18:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yehova anati kwa Aroni, Iwe ndi ana ako amuna ndi banja la kholo lako pamodzi ndi iwe muzisenza mphulupulu ya malo opatulika; ndipo iwe ndi ana ako amuna pamodzi ndi iwe musenze mphulupulu ya nchito yanu ya nsembe.

2. Ndiponso abale ako, pfuko la Alevi, pfuko la kholo lako, uwayandikizitse pamodzi ndi iwe, kuti aphatikane ndi iwe, ndi kukutumikira; koma iwe ndi ana ako pamodzi ndi iwe mukhale ku khomo la cihema ca mboni.

3. Ndipo asunge udikiro wako, ndi udikiro wa cihema conse; koma asayandikize zipangizo za malo opatulika, ndi guwa la nsembe, kuti mungafe, iwo ndi inu.

4. Koma aziphatikana nawe, nazisunga udikiro wa cihema cokomanako, kucita nchito yonse ya cihema; koma mlendo asayandikize inu.

5. Ndipo musunge udikiro wa malo opatulika, ndi udikiro wa guwa la nsembe; kuti pasakhalenso mkwiyo pa ana a Israyeli.

6. Ndipo Ine, taonani, ndinatenga abale anu Alevi kuwacotsa pakati pa ana a Israyeli; ndiwo mphatso yanu, yopatsidwa kwa Yehova, kucita nchito ya cihema cokomanako.

7. Ndipo iwe ndi ana ako amuna pamodzi ndi iwe mucite nchito yanu ya nsembe, pa zonse za ku guwa la nsembe, ndi za m'kati mwa nsaru yocinga; ndipo mutumikire; ndikupatsani nchito yanu ya nsembe, utumiki wopatsika kwaulere; koma mlendo wakuyandikiza amuphe.

Werengani mutu wathunthu Numeri 18