Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 16:1-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma Kora, mwana wa Izara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, anatenga Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, ndi Oni mwana wa Peleti, ana a Rubeni;

2. ndipo anauka pamaso pa Mose, pamodzi ndi amuna: mazana awiri mphambu makumi asanu a ana a Israyeli, ndiwo akalonga a khamulo, oitanidwa a msonkhano, amuna omveka.

3. Ndipo anasonkhana motsutsana pa Mose ndi Aroni, nanena nao, Mukula mphamvu inu, pakuti khamu lonse nlopatulika, onsewa, ndipo Yehova ali pakati pao; mudzikuza bwanji pa msonkhano wa Yehova?

4. Pamene Mose anamva ici anagwa nkhope yace pansi;

5. nanena ndi Kora ndi khamu lace lonse, ndi kuti, M'mawa Yehova adzatizindikiritsa anthu ace ndi ayani, wopatulika ndani, amene adzamsendeza pafupi pa iye; ndi iye amene anamsankha adzamsendeza pafupi pa iye.

6. Citani ici; dzitengereni mbale za zofukiza, Kora, ndi khamu lace lonse;

7. nimuikemo moto, muikenso cofukiza pamenepo, pamaso pa Yehova, mawa; ndipo kudzali kuti amene Yehova amsankha, wopatulika ndiye; mwakula mphamvu, inu ana a Levi.

8. Ndipo Mose ananena ndi Kora, Tamvani tsono, inu ana a Levi;

9. kodi muciyesa cinthu cacing'ono, kuti Mulungu wa Israyeli anakusiyanitsani ku khamu la Israyeli, kukusendezani pafupi pa iye, kucita nchito ya kacisi wa Yehova, ndi kuima pamaso pa khamu kuwatumikira;

10. ndi kuti anakusendeza iwe, ndi abale ako onse, ana a Levi, pamodzi ndi iwe? ndipo kodi mufunanso nchito ya nsembe?

11. Cifukwa cace, iwe ndi khamu lonse mwasonkhana kutsutsana ndi Yehova; ndipo Aroniyo ndani, kuti mudandaule pa iye?

12. Ndipo Mose anatuma kukaitaniza Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu; koma anati, Sitifikako:

13. kodi ndi cinthu cacing'ono kuti watikweza kuticotsa m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi, kutipha m'cipululu; koma udziyesanso ndithu kalonga wa ife?

14. Ndiponso sunatilowetsa m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi, kapena kutipatsa colowa ca minda, ndi minda yamphesa; kodi udzakolowola amuna awa maso ao? Sitifikako.

15. Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira copereka cao; siodinalanda buru wao mmodzi, kapena kucitira coipa mmodzi wa iwowa.

16. Ndipo Mose anati kwa Kora, Iwe ndi khamu lako lonse mukhale pamaso pa Yehova mawa, iwe ndi iwowa, ndi Aroni;

Werengani mutu wathunthu Numeri 16