Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Numeri 11:19-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Simudzadya tsiku limodzi, kapena masiku awiri, kapena masiku asanu, kapena masiku khumi, kapena masiku makumi awiri;

20. koma mwezi wamphumphu, kufikira ibwera m'mphuno mwako, ndi kuti ufukidwa nayo, pakuti mwakaniza Yehova wakukhala pakati pa inu, ndi kulira pamaso pace, ndi kuti, Tinaturukiranji m'Aigupto?

21. Ndipo Mose anati, Anthu amene ndiri pakati pao, ndiwo zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda pansi, ndipo Inu mwanena, Ndidzawapatsa nyama, kuti adye mwezi wamphumphu.

22. Kodi adzawaphera magulu a nkhosa ndi ng'ombe, kuwakwanira? kapena kodi nsomba zonse za m'nyanja zidzawasonkhanira pamodzi, kuwakwanira?

23. Ndipo Yehova anati kwa Mose, Kodi dzanja la Mulungu lafupikira? tsopano udzapenya ngati mau anga adzakucitikira kapena iai.

24. Ndipo Mose anaturuka, nauza anthu mau a Yehova; nasonkhanitsa akuru a anthu makumi asanu ndi awiri, nawaimika pozungulira pa cihema.

25. Ndipo Yehova anatsika mumtambo, nanena nave, natengako mzimu uli pa iye, nauika pa akuru makumi asanu ndi awiri; ndipo kunali kuti pokhala mzimu pa iwowa, ananenera; koma osabwerezanso.

26. Koma amuna awiri anatsalira m'cigono, dzina la wina ndiye Elidadi, dzina la mnzace ndiye Medadi; ndipo mzimuwo unakhala pa iwo; iwo ndiwo mwa oitanidwawo, koma sanaturuka kumka kucihema; ndipo ananenera m'cigono.

27. Ndipo anathamanga anyamata, nauza Mose, nati, Elidadi ndi Medadi alikunenera m'cigono.

28. Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose kuyambira ubwana wace, anayankha nati, Mose, mfumu yanga, aletseni.

29. Koma Mose anati kwa iye, Kodi ucita nsanje nao cifukwa ca ine? Mwenzi anthu onse a Yehova atakhala aneneri! mwenzi Yehova atawaikira mzimu wace!

30. Ndipo Mose ndi akulu onse a Israyeli anasonkhana kucigono.

31. Ndipo kudacokera mphepo kwa Yehova, nidza nazo zinziri zocokera kunyanja, nizitula kucigono, ulendo wa tsiku limodzi dera lino, ndi ulendo wa tsiku limodzi dera lina, pozungulira pa cigono, ndipo zinabisa nthaka ngati muyeso wa mikono iwiri.

32. Ndipo anthu anauka tsiku lonselo, ndi usiku wace wonse, ndi mawa lace lonse, nakusa zinzirizo; wokusa pang'ono anakusa zodzaza mahomeri khumi; ndipo anadziyanikira izi pozungulira pa cigono.

33. Nyamayi ikali pakati pa mano, asanaitafune, Mulungu anapsa mtima pa anthuwa, ndipo Yehova anawakantha anthu ndi kukantha kwakukuru ndithu.

Werengani mutu wathunthu Numeri 11