Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 9:7-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Inu ndinu Yehova Mulungu amene munasankha Abramu ndi kumturutsa m'Uri wa Akasidi, ndi kumucha dzina lace Abrahamu;

8. ndipo munampeza mtima wace wokhulupirika pamaso panu, nimunapangana naye kumpatsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, ndi Aperizi, ndi Ayebusi, ndi Agirigasi, kulipereka kwa mbumba zace; ndipo mwakwaniritsa mau anu, popeza Inu ndinu wolungama.

9. Ndipo munapenya msauko wa makolo athu m'Aigupto, nimunamva kupfuula kwao ku Nyanja Yofiira,

10. nimunacitira zizindikilo ndi zodabwiza Farao ndi akapolo ace onse, ndi anthu onse a m'dziko lace; popeza munadziwa kuti anawacitira modzikuza; ndipo munadzibukitsira dzina monga lero lino.

11. Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m'madzi olimba.

12. Munawatsogoleranso usana ndi mtambo woti njo, ndi moto tolo usiku, kuwaunikira m'njira akayendamo.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 9