Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 8:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anthu onse anasonkhana ngati munthu mmodzi ku khwalala liri ku cipata ca kumadzi, namuuza Ezara mlembi atenge buku la cilamulo ca Mose, cimene Yehova adalamulira Israyeli.

2. Ndipo Ezara wansembe anabwera naco cilamulo pamaso pa msonkhano, ndiwo amuna ndi akazi, ndi yense wakumva ndi kuzindikira tsiku loyamba la mwezi wacisanu ndi ciwiri.

3. Nawerenga m'menemo pa khwalala liri ku cipata ca kumadzi kuyambira mbanda kuca kufikira msana, pamaso pa amuna ndi akazi, ndi iwo okhoza kuzindikira; ndi anthu onse anacherera khutu buku la cilamulo.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 8