Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 4:15-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo kunali, pakumva adani athu kuti cinadziwika nafe, ndi kuti Mulungu adapititsa pacabe uphungu wao, tinabwera tonse kumka kulinga, yense ku nchito yace.

16. Ndipo kuyambira pamenepo gawo lina la anyamata anga anagwira nchito, ndi gawo ina linagwira nthungo, zikopa, ndi mauta, ndi maraya acitsulo; ndi akuru anali m'mbuyo mwa nyumba yonse ya Yuda.

17. Iwo omanga linga, ndi iwo osenza katundu, posenza, anacita ali yense ndi dzanja lace lina logwira nchito, ndi lina logwira cida;

18. ndi omanga linga ali yense anamangirira lupanga lace m'cuuno mwace, nagwira nchito motero. Ndipo woomba lipenga anali ndi ine.

19. Ndipo ndinati kwa aufulu, ndi olamulira, ndi anthu otsala, Nchito ndiyo yocuruka ndi yacitando, ndi ife tiri palace palace palingapo, yense azana ndi mnzace;

20. pali ponse mukumva mau a lipenga, musonkhanire komweko kwa ife; Mulungu wathu adzatigwirira nkhondo.

21. Momwemo tinalikugwira nchito; gawo lina la iwo linagwira nthungo kuyambira mbanda kuca mpaka zaturuka nyenyezi.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 4