Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 3:4-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Ndi pambali pao anakonza Meremoti mwana wa Uliya, mwana wa Kozi. Ndi pambali pao anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabele. Ndi pambali pao anakonza Zadoki mwana wa Baana.

5. Ndi pambali pao anakonza Atekoa; koma omveka ao sanapereka makosi ao ku nchito ya Mbuye wao.

6. Ndi cipata cakale anacikonza Yoyada mwana wa Paseya; ndi Mesulamu mwana wa Besodeya anamanga mitanda yace, ndi kuika zitseko zace, ndi zokowera zace, ndi mipingiridzo yace.

7. Ndi pambali pao anakonza Melatiya Mgibeoni, ndi Yadoni Mheronoti, ndi amuna a ku Gibeoni, ndi a ku Mizipa, wa ulamuliro wa ciwanga tsidya lino la mtsinje.

8. Pambali pace anakonza Uziyeli mwana wa Haraya, wa iwo osula golidi. Ndi padzanja pace anakonza Hananiya, wa iwo osanganiza zonunkhira; nalimbikitsa Yerusalemu mpaka linga lacitando.

9. Ndi pambali pao anakonza Refaya mwana wa Huri, ndiye mkuru wa dera lina la dziko la Yerusalemu.

10. Ndi pambali pao anakonza Yedaya mwana wa Harumafi, pandunji pa nyumba yace. Ndi pambali pace anakonza Hatusi mwana wa Hasabineya.

11. Malikiya mwana wa Harimu, ndi Hasubi mwana wa Pahati-Moabu, anakonzal gawo lina, ndi nsanja ya ng'anjo.

12. Ndi pambali pace anakonza Salumu mwana wa Halohesi, mkuru wa dera lina la dziko la Yerusalemu, iye ndi ana ace akazi.

13. Cipata ca kucigwa anacikonza Hanini; ndi okhala m'Zanowa anacimanga, naika zitseko zace, zokowera zace, ndi mipiringidzo yace; ndiponso mikono cikwi cimodzi ca lingalo mpaka ku cipata ca kudzala.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 3