Ndi cipata cakale anacikonza Yoyada mwana wa Paseya; ndi Mesulamu mwana wa Besodeya anamanga mitanda yace, ndi kuika zitseko zace, ndi zokowera zace, ndi mipingiridzo yace.