Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 13:3-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo kunali, atamva cilamuloco, anasiyanitsa pa Israyeli anthu osokonezeka onse.

4. Cinkana ici, Eliasibu wansembe, woikidwa asunge zipinda za nyumba ya Mulungu wathu, anacita cibale ndi Tobiya,

5. namkonzera cipinda cacikuru, kumene adasungira kale zopereka za ufa, libano, ndi zipangizo, ndi limodzi limodzi la magawo khumi a tirigu, vinyo, ndi mafuta, zolamutidwira Alevi, ndi oyimbira, ndi odikira, ndi nsembe zokweza za ansembe.

6. Koma pocitika ici conse sindinakhala ku Yerusalemu; pakuti caka ca makumi atatu ndi caciwiri ca Aritasasta mfumu ya Babulo ndinafika kwa mfumu, ndipo atapita masiku ena ndinapempha mfumu indilole;

7. ndipo ndinafika ku Yerusalemu, ndi kuzindikira coipa anacicita Eliasibu, cifukwa ca Tobiya, ndi kumkonzera cipinda m'mabwalo a nyumba ya Mulungu.

8. Ndipo ndinaipidwa naco kwambiri, motero ndinataya kubwalo akatundu onse a m'nyumba ya Tobiya, kuwacotsa m'cipindamo.

9. Pamenepo ndinalamulira, ndipo anayeretsa zipindazo; ndipo ndinabwezeramonso zipangizo za nyumba ya Mulungu, pamodzi ndi zopereka za ufa ndi libano.

10. Ndinazindikiranso kuti sanapereka kwa Alevi magawo ao; m'mwemo Alevi ndi oyimbira adathawira yense ku munda wace.

11. Potero ndinatsutsana nao olamulira, ndinati, Yasiyidwiranji nyumba ya Mulungu? Ndipo ndinawasonkhanitsa, ndi kuwafka m'malo mwao.

12. Ndi Ayuda onse anabwera nalo limodzi limodzi la magawo khumi a tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ku nyumba za cuma.

13. Ndinaikanso osunga cuma, asunge nyumba za cuma: Selemiya wansembe, ndi Zadoki mlembi; ndi wa Alevi, Pedaya; ndi wakuwathandiza, Hanani mwana wa Zakuri, mwana wa Mataniya; popeza anayesedwa okhulupirika ndi udindo wao, ndiwo kugawira abale ao.

14. Mundikumbukile Mulungu wanga mwa ici, nimusafafanize zokoma zanga ndinazicitira nyumba ya Mulungu wanga, ndi maudikiro ace.

15. Masiku awa ndinaona ku Yuda ena akuponda mphesa m'coponderamo dzuwa la Sabata, ndi akubwera nayo mitolo ya tirigu, ndi kuisenzetsa pa aburu; momwemonso vinyo, mphesa, ndi nkhuyu, ndi zosenza ziri zonse, zimene analowa nazo m'Yerusalemu dzuwa la Sabata, ndipo ndinawacitira umboni wakuwatsutsa tsikuti anagulitsa zakudya.

16. Anakhalanso m'menemo a ku Turo, obwera nazo nsomba, ndi malonda ali onse, nagulitsa dzuwa la Sabata kwa ana a Yuda ndi m'Yerusalemu.

17. Pamenepo ndinatsutsana nao aufulu a Yuda, ndinanena nao, Cinthu canji coipa ici mucicita, ndi kuipsa naco dzuwa la Sabata?

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 13