Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 12:43-47 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

43. Ndipo anaphera nsembe zambiri tsiku lija, nasekerera; pakuti Mulungu anawakondweretsa ndi cimwemwe cacikuru; ndi akazi omwe ndi ana anakondwera; ndi cikondwerero ca Yerusalemu cinamveka kutali.

44. Ndipo tsiku lomwelo anaika anthu asunge zipinda za cuma, za nsembe zokweza, za zipatso zoyamba, ndi za limodzi limodzi la magawo khumi, kulonga m'mwemo, monga mwa minda ya midzi, magawo onenedwa ndi cilamulo, akhale a ansembe ndi Alevi; popeza Yuda anakondwera nao ansembe ndi Alevi lakuimirirako.

45. Ndipo iwo anasunga udikiro wa Mulungu wao, ndi udikiro wa mayeretsedwe; momwemonso oyimbira ndi odikira, monga mwa lamulo la Davide ndi la Solomo mwana wace.

46. Pakuti m'masiku a Davide ndi Asafu kalelo kunali mkuru wa oyimbira, ndi wa nyimbo zolemekeza ndi zoyamikira Mulungu.

47. Ndi Aisrayeli onse m'masiku a Zerubabele, ndi m'masiku a Nehemiya, anapereka magawo a oyimbira ndi odikira, monga mudafunika tsiku ndi tsiku; nawapatulira Alevi; ndi Alevi anawapatulira ana a Aroni.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 12