Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 12:38-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

38. Ndi gulu lina la oyamikira linamuka mokomana nao, ndi ine ndinawatsata, pamodzi ndi limodzi la magawo awiri la anthu palinga, napitirira pa nsanja ya ng'anjo, mpaka ku linga lacitando;

39. ndi pamwamba pa cipata ca Efraimu, ndi ku cipata cakale, ndi ku cipata cansomba, ndi nsanja ya Hananeli, ndi nsanja ya Hameya, mpaka ku cipata cankhosa; ndipo anaima ku cipata cakaidi.

40. Atatero, magulu awiriwo a iwo oyamikira anaima m'nyumba ya Mulungu, ndipo ine ndi limodzi la magawo awiri a olamulira pamodzi ndi ine;

41. ndi ansembe, Eliakimu, Maaseya, Minyamini, Mikaya, Elioenai, Zekariya, ndi Hananiya, ali nao malipenga;

42. ndi Maaseya, ndi Semaya, ndi Eleazara, ndi Uzi, ndi Yehohanana, ndi Malikiya, ndi Elamu, ndi Ezeri. Ndipo oyimbira anayimbitsa Yeziraya ndiye woyang'anira wao.

43. Ndipo anaphera nsembe zambiri tsiku lija, nasekerera; pakuti Mulungu anawakondweretsa ndi cimwemwe cacikuru; ndi akazi omwe ndi ana anakondwera; ndi cikondwerero ca Yerusalemu cinamveka kutali.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 12