Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 10:27-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Maluki, Harimu, Baana.

28. Ndi anthu otsala, ansembe, Alevi, odikira, oyimbira, Anetini, ndi onse anadzisiyanitsawo pa mitundu ya anthu a m'dziko kutsata cilamulo ca Mulugu, akazi ao, ana ao amuna ndi akazi, yense wodziwa ndi wozindikira,

29. amenewa anaumirira abale ao, omveka ao, nalowa m'temberero ndi lumbiro, kuti adzayenda m'cilamulo ca Mulungu anacipereka Mose mtumiki wa Mulungu, ndi kuti adzasunga ndi kucita zonse atilamulira Yehova Ambuye wathu, ndi maweruzo ace, ndi malemba ace;

30. ndi kuti sitidzapereka ana athu akazi kwa mitundu ya anthu a m'dziko, kapena kutengera ana athu amuna ana ao akazi;

31. ndipo mitundu ya anthu a m'dziko akabwera nao malonda, ngakhale tirigu, dzuwa la Sabata, kutsata malonda, sitidzagulana nao dzuwa la Sabata, kapena dzuwa lina lopatulika, ndi kuti tidzaleka caka cacisanu ndi ciwiri ndi mangawa ali onse.

32. Tinadziikiranso malamulo, kuti tizipereka caka ndi caka limodzi la magawo atatu a sekeli ku nchito ya nyumba ya Mulungu wathu;

33. kuliperekera mkate woonekera, ndi nsembe yaufa yosaleka, ndi nsembe yopsereza yosaleka, ya masabata, ya pokhala miyezi, kuliperekera nyengo zoikika ndi zopatulikira, ndi nsembe za zolakwa za kutetezera Israyeli zoipa, ndi nchito zonse za nyumba ya Mulungu wathu.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 10