Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Mlaliki 2:19-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo ndani adziwa ngati adzakhala wanzeru pena citsiru? Koma adzalamulira nchito zanga zonse ndinasauka nazo, ndi kuzigwira mwanzeru kunja kuno. Icinso ndi cabe.

20. Ndipo ndinatembenuka ndi kukhululuka za nchito zanga zonse ndasauka nazo kunja kuno.

21. Pakuti pali munthu wina agwira nchito mwanzeru ndi modziwa nadzipinduliramo; koma adzapereka gawo lace kwa munthu amene sanagwirapo nchito. Icinso ndi cabe ndi coipa cacikuru.

22. Pakuti munthu ali ndi ciani m'nchito zace zonse, ndi m'kusauka kwa mtima wace amasauka nazozo kunja kuno?

23. Pakuti masiku ace onse ndi zisoni, bvuto lace ndi kumliritsa; ngakhale usiku mtima wace supuma. Icinso ndi cabe.

24. Kodi si cabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wace, zabwino m'nchito yace? icinso ndinacizindikira kuti cicokera ku dzanja la Mulungu.

25. Pakuti ndani angadye ndi kufulumirako, koposa ine.

26. Pakuti yemwe Mulungu amuyesa wabwino ampatsa nzeru ndi cidziwitso ndi cimwemwe; koma wocimwa amlawitsa bvuto la kusonkhanitsa ndi kukundika, kuti aperekere yemwe Mulungu amuyesa wabwino. Icinso ndi cabe ndi kungosautsa mtima.

Werengani mutu wathunthu Mlaliki 2