Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Masalmo 40:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Kuyembekeza ndayembekeza Yehova;Ndipo anandilola, namva kupfuula kwanga.

2. Ndipo anandikweza kunditurutsa m'dzenje la citayiko, ndi m'thope la pacithaphwi;Nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.

3. Ndipo anapatsa Nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, cilemekezo ca kwa Mulungu wanga;Ambiri adzaciona, nadzaopa,Ndipo adzakhulupirira Yehova.

4. Wodala munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika;Wosasamala odzikuza, ndi opatukira kubodza.

5. Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwiza zanu mudazicita nzambiri,Ndipo zolingirira zanu za pa ife;Palibe wina wozifotokozera Inu;Ndikazisimba ndi kuzichula, Zindicurukira kuziwerenga.

6. Nsembe ndi copereka simukondwera nazo;Mwanditsegula makutu:Nsembe yopsereza ndi yamacimo simunapempha.

7. Pamenepo ndinati, Taonani, ndadza;M'buku mwalembedwa za Ine:

8. Kucita cikondwero canu kundikonda, Mulungu wanga;Ndipo malamulo anu ali m'kati mwamtima mwanga.

9. Ndalalikira cilungamo mu msonkano waukuru;Onani, sindidzaletsa milomo yanga,Mudziwa ndinu Yehova.

10. Cilungamo canu sindinacibisa m'kati mwamtima mwanga;Cikhulupiriko canu ndi cipulumutso canu ndinacinena;Cifundo canu ndi coonadi canu sindinacibisira msonkhano waukuru.

11. Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu:Cifundo canu ndi coonadi canu zindisunge cisungire.

12. Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga,Zocimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya;Ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandicokera mtima.

13. Ndikupemphani, Yehova, ndilanditseni:Fulumirani kudzandithandiza, Yehova.

14. Acite manyazi nadodomeIwo akulondola moyo wanga kuti auononge:Abwerere m'mbuyo, nacite manyazi iwo okondwera kundicitira coipa.

15. Apululuke, mobwezera manyazi aoAmene anena nane, Hede, hede.

Werengani mutu wathunthu Masalmo 40