Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Maliro 1:6-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Ulemu wace wonse wamcokera mwana wamkazi wa Ziyoni;Akalonga ace asanduka nswala zosapeza busa,Anayenda opanda mphamvu pamaso pa wompitikitsa.

7. M'masiku a msauko wace ndi kusocera kwaceYerusalemu ukumbukira zokondweretsa zace zonse zacikhalire;Pogwidwa anthu ace ndi mdaniyo popanda wakuupulumutsa,Adaniwo anamuona naseka mwacipongwe mabwinja ace.

8. Yerusalemu wacimwa kwambiri; cifukwa cace wasanduka cinthu conyansa;Onse akuulemekeza aupeputsa, pakuti auona wamarisece;Inde, uusa moyo, nubwerera m'mbuyo.

9. Udio wace unali m'nsaru zace; sunakumbukira citsiriziro cace;Cifukwa cace watsika mozizwitsa; ulibe wakuutonthoza;Taonani Yehova, msauko wanga, pakuti mdaniyo wadzikuzayekha.

10. Amaliwongo atambasulira manja ao pa zokondweretsa zace zonse;Pakuti waona amitundu atalowa m'malo ace opatulika,Amene munalamulira kuti asalowe mumsonkhano mwanu.

11. Anthu ace onse ausa moyo nafunafuna mkate;Ndi zokondweretsa zao agula zakudya kuti atsitsimutse moyo wao;Taonani, Yehova, nimupenye; pakuti ndasanduka wonyansa.

12. Kodi muyesa cimeneci cabe, nonsenu opita panjira?Penyani nimuone, kodi ciripo cisoni cina ngati cangaci amandimvetsa ine,Cimene Yehova wandisautsa naco tsiku la mkwiyo wace waukali?

13. Anatumiza moto wocokera kumwamba kulowa m'mafupa anga, unawagonjetsa;Wachera mapazi anga ukonde, wandibwezera m'mbuyo;Wandipululutsa ndi kundilefula tsiku lonse.

14. Gori la zolakwa zanga lamangidwa ndi dzanja lace;Zalukidwa, zakwera pakhosi panga; iye wakhumudwitsa mphamvuyanga;Ambuye wandipereka m'manja mwao, sindithai kuwalaka.

Werengani mutu wathunthu Maliro 1