M'masiku a msauko wace ndi kusocera kwaceYerusalemu ukumbukira zokondweretsa zace zonse zacikhalire;Pogwidwa anthu ace ndi mdaniyo popanda wakuupulumutsa,Adaniwo anamuona naseka mwacipongwe mabwinja ace.