14. Gori la zolakwa zanga lamangidwa ndi dzanja lace;Zalukidwa, zakwera pakhosi panga; iye wakhumudwitsa mphamvuyanga;Ambuye wandipereka m'manja mwao, sindithai kuwalaka.
15. Ambuye wapepula ngwazi zanga zonse pakati panga;Waitanira msonkhano pa ine kuti uphwanye anyamata anga,Ambuye wapondereza namwaliyo, mwana wamkazi wa Ziyoni, monga mopondera mphesa.
16. Cifukwa ca zimenezi ndilira; diso langa, diso langatu likudza madzi:Pakuti wonditonthoza, wotsitsimutsa moyo wanga, anditarikira;Ana anga asungulumwa, pakuti adaniwo apambana.
17. Ziyoni atambasula manja ace, palibe wakumtonthoza;Yehova walamulira kuti omzungulira Yakobo akhale adani ace;Yerusalemu wasanduka cinthu conyansa pakati pao.
18. Yehova ali wolungama; pakuti ndapikisana ndi m'kamwa mwace:Mudtvetu, mitundu ya anthu nonsenu, nimuone cisoni canga;Anamwali ndi anyamata anga atha kulowa m'ndende.
19. Ndinaitanaakundikondawokoma anandinyenga;Ansembe ndi akulu anga anamwalira m'mudzimu,Alikufunafuna zakudya zotsitsimutsa miyoyo yao.
20. Onani, Yehova; pakuti ndabvutika, m'kati mwanga mugwedezeka;Mtima wanga wasanduka mwa ine; pakuti ndapikisana nanu ndithu;Kunjako lupanga limangopha ana; m'nyumba muli imfa.
21. Iwo anamva kuti ndiusa moyo, palibe wonditonthoza;Adani anga onse atha kumva msauko wanga, nakondwera kuti mwatero ndinu;Mudzafikitsa tsiku lija mwalichula, ndipo iwowo adzanga ine.
22. Zoipa zao zonse zidze pamaso panu,Muwacitire monga mwandicitira ine cifukwa ca zolakwa zanga zonse,Pakuti ndiusa moyo kwambiri, ndi kulefuka mtima wanga,